Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 34:34 - Buku Lopatulika

Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nthaŵi zonse Moseyo ankati akaloŵa m'chihema kukalankhula ndi Chauta, ankachotsa nsalu yophimba kumaso ija mpaka atatuluka. Tsono atatuluka, ankauza Aisraele aja zonse zimene Chauta wamulamula kuti anene.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa,

Onani mutuwo



Eksodo 34:34
4 Mawu Ofanana  

Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.


Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chichotsedwa.


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.