Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 32:26 - Buku Lopatulika

Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana aamuna onse a Levi anasonkhana kwa iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Moseyo adaimirira pa chipata cha mahema aja ndipo adafuula mokweza nafunsa kuti, “Kodi ndani akufuna Chauta? Bwerani kuno.” Pompo Alevi onse adadzasonkhana kwa iye,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho iye anayima pa chipata cholowera mu msasa ndipo anati, “Aliyense amene ali mbali ya Yehova abwere kwa ine.” Ndipo Alevi onse anapita mbali yake.

Onani mutuwo



Eksodo 32:26
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.


Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.


Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?


Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,


Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake.


Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?