Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 94:16 - Buku Lopatulika

16 Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndani amalimba mtima kuti andimenyere nkhondo ndi anthu oipa? Ndani amaimira mbali yanga, kuti alimbane ndi anthu ochita zoipa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa? Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 94:16
19 Mawu Ofanana  

Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta.


Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.


Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa.


Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?


Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;


Mundilanditse kwa ochita zopanda pake, ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.


Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; chifukwa chake mkono wakewake unadzitengera yekha chipulumutso; ndi chilungamo chake chinamchirikiza.


Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.


Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.


Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.


Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.


Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova, mutemberere chitemberere nzika zake; pakuti sanadzathandize Yehova, kumthandiza Yehova pa achamuna.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa