Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.
Eksodo 32:21 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Mose adafunsa Aroni uja kuti, “Kodi anthu ameneŵa adakuchita zotani iwe, kuti uŵachimwitse koopsa chotere?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose anafunsa Aaroni kuti, “Kodi anthu awa anakuchita chiyani kuti uwachimwitse koopsa chotere?” |
Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.
Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife.
Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele.
ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.
Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele.
Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndilikumva, nchiyani?
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.