Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira.
Eksodo 30:17 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Mose, |
Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira.
Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.
Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.
Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.
Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu.
Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.