2 Mbiri 4:6 - Buku Lopatulika6 Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Adapanganso mabeseni khumi osambiramo. Kumwera adaikako asanu ndipo kumpoto adaikakonso asanu. M'menemo ndimonso ankatsukiramo zinthu zimene ankagwiritsa ntchito popereka nsembe zopsereza. Koma m'thanki lalikulu lija ndimo m'mene ankasambiramo ansembe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Kenaka anapanga mabeseni khumi otsukira zinthu ndipo asanu amawayika mbali ya kummwera, asanu mbali ya kumpoto. Mʼmenemo amatsukiramo zinthu zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nsembe zopsereza koma mbiyamo ndi mʼmene ankasambiramo ansembe. Onani mutuwo |