Eksodo 3:3 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mumtima mwake adati, “Ndipita pafupi, kuti ndikaonetsetse zozizwitsa ndikupenyazi. Chifukwa chiyani chitsambacho sichilikupsa?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?” |
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.
Koma Mose pakuona, anazizwa pa choonekacho; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye,