Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 29:3 - Buku Lopatulika

Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Uziike m'lichero, ndipo ubwere nazo kwa Ine, pamene ukupereka nsembe ng'ombe yamphongo ija ndi nkhosa zija.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija.

Onani mutuwo



Eksodo 29:3
6 Mawu Ofanana  

ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.


Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;


Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.


naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.