Eksodo 28:34 - Buku Lopatulika mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho pakhale khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho pazikhala mphonje imodzi kenaka belu limodzi, kuzungulira mpendero wa mkanjo wonse. |
Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;
Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe.
Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.
Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.
Milomo yako ikunga mbota yofiira, m'kamwa mwako ndi kukoma: Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseri pa chophimba chako.
Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.
Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai, kuti andilange mwambo; ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa, ndi madzi a makangaza anga.
Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;