Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.
Eksodo 28:22 - Buku Lopatulika Upangenso maunyolo pa chapachifuwa ngati zingwe, ntchito yopota, ya golide woona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Upangenso maunyolo pa chapachifuwa ngati zingwe, ntchito yopota, ya golide woona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange timaunyolo ta golide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota mwaluso ngati maukufu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Upange timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. |
Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.
M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo.
ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.
Nupangire pa chapachifuwa mphete ziwiri zagolide, ndi kuzika mphete ziwirizo pansonga zake ziwiri za chapachifuwa.