Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Eksodo 28:16 - Buku Lopatulika Chikhale chaphwamphwa, chopindika, utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chikhale chaphwamphwa, chopindika, utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kukula kwake kukhale kofanana mbali zonse, ndipo chikhale chopinda paŵiri. M'litali mwake chikhale masentimita 23, muufupi mwake chimodzimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kutalika kwake kukhale kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, ndipo chikhale chopinda pawiri. |
Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba;
Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.