Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Eksodo 28:13 - Buku Lopatulika Ndipo upange zoikamo za golide; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo upange zoikamo za golide; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upangenso zoikamo zonga maluŵa agolide, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange zoyikamo za maluwa agolide, |
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pansonga ziwiri za chapachifuwa.
Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.