Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.
Eksodo 28:10 - Buku Lopatulika maina asanu ndi limodzi pamwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pamwala unzake, mwa kubadwa kwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzake, mwa kubadwa kwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mwala umodzi ulembepo maina asanu ndi limodzi, ndipo pa mwala winawo uchitenso chimodzimodzi. Ulembe mainawo motsatana malinga nkubadwa kwa ana a Israelewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo. |
Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.