Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Eksodo 26:9 - Buku Lopatulika Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usoke nsalu zisanu kuti zikhale nsalu imodzi, ndipo zisanu ndi imodzi zinazo zikhalenso nsalu imodzi. Tsono upinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo mophatikiza patsogolo pa chihema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri. |
Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake.
Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.
Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.