Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 26:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Usoke nsalu zisanu kuti zikhale nsalu imodzi, ndipo zisanu ndi imodzi zinazo zikhalenso nsalu imodzi. Tsono upinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo mophatikiza patsogolo pa chihema.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:9
4 Mawu Ofanana  

Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.


Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.


“Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi.


Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa