Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 26:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Upangenso magonga makumi asanu m'mbali mwake mwa nsalu yotsirizira ya chinsalu chimodzi, ndiponso magonga makumi asanu pa nsalu yotsiriza inayo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:10
4 Mawu Ofanana  

Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi.


Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo.


Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri.


Iwo anasokerera zokolowekamo makumi asanu pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Anapanga kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa