Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Eksodo 26:5 - Buku Lopatulika Uziika magango makumi asanu pansalu yochingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uziika magango makumi asanu pa nsalu yochingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka upange timagonga makumi asanu pa nsalu yoyambayo, ndipo timagonga tinanso makumi asanu pa nsalu yachiŵiriyo, kuti timagongato tiyang'anane. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. |
Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.
Anaika magango makumi asanu pansalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake.