Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 26:6 - Buku Lopatulika

6 Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti Kachisi akhale mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono upange ngoŵe zagolide makumi asanu, zolumikizira nsalu ziŵirizo, kuti chipangike chihema chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:6
11 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.


Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri.


Uziika magango makumi asanu pansalu yochingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake.


Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.


chihema, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao;


Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo chihema chinakhala chimodzi.


Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.


Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake;


kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa