Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.
Mafulemuwo uŵakute ndi golide, ndi kulonganso mphete zagolide m'mafulemuwo kuti agwirizire mitanda ija, ndipo mitandayo ikhale yokutidwa ndi golide.
Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.
Ndipo m'kati mwa chipindacho, m'litali mwake munali mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golide wayengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza.
Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golide mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali chakuno cha chipinda chamkati analikuta ndi golide.
Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome.
Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo.
Ndipo uutse chihema monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m'phiri.