Eksodo 26:27 - Buku Lopatulika ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ina ya chihema, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya chihema cha kumbuyo kumadzulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya Kachisi ya kumbuyo kumadzulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndi isanu inanso pa mafulemu a mbali ina. Pakhalenso mitanda isanu pa mafulemu akuzambwe chakumbuyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. |