Eksodo 26:18 - Buku Lopatulika Ndipo uzipanga matabwa a chihema, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwera, kumwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uzipanga matabwa a Kachisi, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwera, kumwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popanga mafulemuwo, ku mbali yakumwera, upange makumi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho. |
Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a chihema.
Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;