Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwali mkono ndi hafu.
Eksodo 26:17 - Buku Lopatulika Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a chihema. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a Kachisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziŵiri, ndipo mafulemu onse a chihemacho apangidwe ndi matabwa otere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. |
Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwali mkono ndi hafu.
Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;
Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a chihema.
napanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri.