Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.
Eksodo 26:12 - Buku Lopatulika Ndipo chotsalacho pansalu yophimbayo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, itchinge pambuyo pake pa chihemacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chotsalacho pa nsalu za hemalo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, ichinge pambuyo pake pa Kachisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Theka la nsalu yotsalira ija idzalendeŵera kumbuyo kwa chihemacho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho. |
Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.
Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira mu utali wake wa nsalu zophimbazo, itchinge pambali zake za chihemacho, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba.
Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.