Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Eksodo 26:11 - Buku Lopatulika Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Upange zomangira makumi asanu zamkuŵa, ndipo uziike m'magongamo. Choncho uphatikize pamodzi nsalu ziŵirizo, kuti pakhale chihema chimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. |
Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Ndipo chotsalacho pansalu yophimbayo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, itchinge pambuyo pake pa chihemacho.
Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake.
Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.