Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.
Eksodo 26:10 - Buku Lopatulika Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upangenso magonga makumi asanu m'mbali mwake mwa nsalu yotsirizira ya chinsalu chimodzi, ndiponso magonga makumi asanu pa nsalu yotsiriza inayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. |
Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.
Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema.
Anaika magango makumi asanu pansalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake.