Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
Eksodo 22:19 - Buku Lopatulika Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Aliyense wogona ndi nyama aphedwe basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Aliyense wogonana ndi chiweto ayenera kuphedwa. |
Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.
ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;
Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.
Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi.
Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;
Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mzinda, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.
ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziwe, ndi kuitumikira;
Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake,
pamenepo mutulutse mwamunayo kapena mkaziyo, anachita choipacho, kunka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.