Eksodo 22:13 - Buku Lopatulika Ngati chajiwa ndithu, abwere nacho chikhale mboni; asalipe pa chojiwacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ngati chajiwa ndithu, abwere nacho chikhale mboni; asalipe pa chojiwacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati chidajiwa ndi zilombo, atengeko zotsalira zake kuti zikhale mboni, koma asalipire chimene chidajiwa ndi zilombocho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati chinagwidwa ndi zirombo, iye ayenera kubweretsa zotsalira ngati umboni ndipo sadzalipira kanthu. |
Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi mu Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.
Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa.