Amosi 3:12 - Buku Lopatulika12 Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi mu Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi m'Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Zimene akunena Chauta ndi izi: “Monga mbusa amangotolako miyendo iŵiri kapena nsonga ya khutu la nkhosa yake ikajiwa ndi mkango, ndimo m'mene adzapulumukire Aisraele okhala ku Samariya, ngati zidutswa chabe za bedi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Yehova akuti, “Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu, moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli amene amakhala mu Samariya pa msonga za mabedi awo, ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.” Onani mutuwo |