Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 3:11 - Buku Lopatulika

11 Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake padziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake pa dziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nchifukwa chake Ambuye Chauta mau ao ndi aŵa: “Adani adzalizinga dzikolo, malinga ake adzaŵagwetsa, ndipo adzafunkha zonse zam'menemo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi: “Mdani adzalizungulira dzikoli; iye adzagwetsa malinga ako, ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:11
17 Mawu Ofanana  

Ndipo ana aamuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mzinda chifukwa anamuipitsa mlongo wao.


Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.


Sikunatsalira kanthu kosadya iye, chifukwa chake zokoma zake sizidzakhalitsa.


koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za mu Yerusalemu.


Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova.


Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.


Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha.


Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mzinda, ndi zonse zili m'menemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa