Akamtengera mkazi wina, asachepetse chakudya chake, zovala zake, ndi za ukwati zakezake.
Eksodo 21:9 - Buku Lopatulika Koma ngati amtomera mwana wake wamwamuna, amchitire monga kuyenera ana aakazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati amtomera mwana wake wamwamuna, amchitire monga kuyenera ana akazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akaganiza zopatsa mwana wake mkaziyo, azidzamsunga ngati mwana wake wamkazi ndithu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati anamusankha kuti akhale mkazi wa mwana wake, ayenera kumusunga ngati mwana wake wamkazi. |
Akamtengera mkazi wina, asachepetse chakudya chake, zovala zake, ndi za ukwati zakezake.
Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga.