Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe.
Eksodo 21:3 - Buku Lopatulika Akalowa ali yekha azituluka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wake azituluka naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akalowa ali yekha azituluka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wake azituluka naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akakhala kuti anali yekha, adzachokanso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pobwerapo, mkazi wakeyo adzapita naye limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso. |
Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe.
Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha.
Ndipo munthu akagulitsa mwana wake wamkazi akhale mdzakazi, iyeyu asatuluke monga amatuluka anyamata.
Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake.