Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
Eksodo 21:29 - Buku Lopatulika Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati khalidwe lake la ng'ombeyo linali kumangogunda anthu, ndipo mwiniwake adachenjezedwa, koma iye osaimanga, ng'ombeyo ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi, iponyedwe miyala ndithu. Ndipo mwiniwakeyonso aphedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso. |
Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.
Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.