Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
Eksodo 20:22 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Chauta adalamula Mose kuti, “Kauze Aisraele kuti, ‘Mwapenyatu kuti Ine Mulungu ndalankhula nanu ndili kumwamba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. |
Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
Kodi pali mtundu wa anthu udamva mau a mulungu wina akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo?
Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo padziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.
ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.
Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?