Eksodo 2:8 - Buku Lopatulika Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Chabwino, pita.” Mlongo wakeyo adapita nakaitana amai ake a mwanayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Inde, pita.” Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. |
Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?
Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa.
Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.