Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Eksodo 2:4 - Buku Lopatulika Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mlongo wake wa mwanayo adaimirira pafupi namangopenyetsetsa, kuti aone zimene zimchitikire mwanayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mlongo wake wa mwanayo anayima pataliko kuti aone chimene chidzamuchitikira mwanayo. |
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi mu Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.