Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Eksodo 18:9 - Buku Lopatulika Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yetero adakondwa kwambiri ndi ntchito zabwino zimene Chauta adaachitira Aisraele pakuŵapulumutsa kwa Aejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto. |
Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.
Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.
Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani chifukwa cha iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.