Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 18:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yetero adakondwa kwambiri ndi ntchito zabwino zimene Chauta adaachitira Aisraele pakuŵapulumutsa kwa Aejipito.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:9
8 Mawu Ofanana  

Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo, ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa. Bwerera kwa Ine, popeza ndakupulumutsa.”


Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi; fuwula, iwe dziko lapansi. Imbani nyimbo, inu mapiri, inu nkhalango ndi mitengo yonse, chifukwa Yehova wawombola Yakobo, waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.


Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova, ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa. Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira. Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake Yehova wachitira nyumba ya Israeli zinthu zabwino zambiri.


“Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye, inu nonse amene mumakonda Yerusalemu, kondwera nayeni kwambiri, nonse amene mumamulira.


Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni.


Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.


Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.


Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa