Eksodo 18:13 - Buku Lopatulika Ndipo kunatero kuti m'mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunatero kuti m'mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake Mose adayamba kuweruza milandu ya anthu. Ndipo anthuwo ankabwera ndi milandu yao kwa Moseyo kuyambira m'maŵa mpaka usiku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. |
Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?
Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m'chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo.
Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira.
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.
Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.