Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 3:12 - Buku Lopatulika

12 Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Anthu a mitundu yonse akonzeke ndipo abwere ku chigwa cha Yehosafati. Pakuti kumeneko ndidzaweruza anthu a mitundu yonse, ochokera ku mbali zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Mitundu ya anthu idzuke; ipite ku Chigwa cha Yehosafati, pakuti kumeneko Ine ndidzakhala ndikuweruza anthu a mitundu yonse yozungulira.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 3:12
17 Mawu Ofanana  

Ndi tsiku lachinai anasonkhana m'chigwa cha Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Beraka, mpaka lero lino.


Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.


Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.


Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.


Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.


Katundu wa chigwa cha masomphenya. Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamatsindwi?


Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu.


Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda mu Israele, chigwa cha opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wake wonse, nadzachitcha, Chigwa cha unyinji wa Gogi.


Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu.


ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.


Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.


Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa