nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha,
Eksodo 17:16 - Buku Lopatulika nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleke m'mibadwomibadwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleke m'mibadwomibadwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adati, “Kwezetsani mbendera ya Chauta! Chauta adzapitirirabe kumenya nkhondo ndi Aamaleke mpaka muyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anati, “Kwezani mbendera ya Yehova. Yehova adzachitabe nkhondo ndi mibado yonse ya Aamaleki.” |
nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha,
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?
Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?