Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:49 - Buku Lopatulika

49 Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 “Chauta akuti, ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 “ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:49
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.


Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.


Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.


Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena mu Yerusalemu.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa