Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.
Eksodo 16:26 - Buku Lopatulika Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutole chakudya pa masiku asanu ndi limodzi. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku la Sabata, chakudyacho sichidzapezeka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muzitola chakudya masiku asanu ndi limodzi koma tsiku la chisanu ndi chiwiri ndi la Sabata, simukapeza chilichonse kunjaku.” |
Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.
Atero Ambuye Yehova, Pa chipata cha bwalo lam'kati choloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.
Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.