Eksodo 16:18 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalire, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowe; yense anaola monga mwa njala yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono atayesa ndi muyeso wa malita aŵiri, adaona kuti amene adaatola tambiri, sitidaŵatsalireko, amene adaatola pang'ono, sitidaŵathere. Aliyense adangotola tokwanira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya. |
Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.