Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga mu Mara.
Eksodo 15:23 - Buku Lopatulika Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a pa Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adakafika ku Mara, koma kumeneko madzi ake anali oŵaŵa, kotero kuti sadathe kuŵamwa. Nchifukwa chake malowo adaŵatcha kuti Mara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara). |
Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga mu Mara.
Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.