Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?
Eksodo 14:6 - Buku Lopatulika Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Farao adakonzetsa galeta lake lankhondo, ndipo adauza asilikali ake kuti apite naye limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anakonzetsa galeta lake ndipo ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake. |
Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?
napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse.
Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.