Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Eksodo 12:24 - Buku Lopatulika Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muziŵamvera malamulo ameneŵa inuyo ndi ana anu mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Muzimvera malamulo amenewa kwa muyaya, inu ndi zidzukulu zanu. |
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Ndipo muzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.
Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m'dziko limene Yehova adzakupatsani, monga analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku.
Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.