Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.
Eksodo 1:18 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana amunawo akhale ndi moyo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mfumu ija idaŵaitana azamba aja niŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵaleka ana aamuna osaŵapha?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mfumu ya Igupto inayitanitsa azamba aja ndi kuwafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? Bwanji mwasiya ana aamuna kuti akhale ndi moyo?” |
Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.
Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.
Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.