2 Samueli 13:28 - Buku Lopatulika28 Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201428 Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa28 Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero28 Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.” Onani mutuwo |