chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira chipangano chake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita.
Danieli 9:10 - Buku Lopatulika sitinamvere mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife sitinamvere Yehova Mulungu wathu kapena kusunga malamulo ake amene anatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki ake. |
chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira chipangano chake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita.
Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa;
ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;
sitinamvere atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko.