Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 9:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ife sitinamvere Yehova Mulungu wathu kapena kusunga malamulo ake amene anatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 sitinamvere mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 9:10
8 Mawu Ofanana  

Izi zinachitika chifukwa sanamvere zonena za Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula. Iwo sanamvere malamulowo kapena kuwagwiritsa ntchito.


Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa.


Iwo analowa nʼkulitenga kukhala lawo, koma sanamvere Inu kapena kutsatira lamulo lanu; ndipo sanachite zomwe munawalamula. Choncho inu mwawagwetsera masautso onsewa.”


Sitinamvere aneneri atumiki anu, amene anayankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, makolo athu, ndi kwa anthu onse a mʼdziko.


Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa